Pitani ku nkhani yake

ZIMENE ACHINYAMATA AMADZIFUNSA

Kodi Ndithetse Chibwenzichi?—Gawo 1

Kodi Ndithetse Chibwenzichi?—Gawo 1

 Nthawi zina zimakhala bwino kuthetsa chibwenzi. Taonani zimene zinachitikira mtsikana wina dzina lake Jill. Iye ananena kuti: “Poyamba ndinkaona kuti mnyamata amene ndinali naye pachibwenzi amandiganizira chifukwa nthawi zonse ankada nkhawa ndi kumene ndinali, zimene ndimachita komanso anthu amene ndinali nawo. Koma zinafika pakuti ankangofuna kuti ndizingocheza ndi iyeyo basi. Moti ankachita nsanje ngakhale ndikamacheza ndi anthu akwathu makamaka bambo anga. Nditathetsa chibwenzi, ndinachita kumva ngati ndatula chimwala cholemera chimene ndinasenza.”

 Nayenso Sarah anakumana ndi zinthu zofanana ndi zimene zinachitikira Jill. Iye anayamba kuzindikira kuti mnyamata amene anali naye pachibwenzi dzina lake John, anali wachipongwe, wovuta komanso wamwano. Sarah ananena kuti: “Nthawi ina tinagwirizana kuti adzanditenge kunyumba kuti tipite kwinakwake. Iye anachedwa ndi maola atatu. Ngakhale kuti mayi anga ndi amene anamutsegulira chitseko, sanawalankhule koma anangondiuza kuti: ‘Tiye tizipita tachedwa.’ M’malo monena kuti ‘ndachedwa’ ananena kuti ‘tachedwa.’ Iye anayenera kupepesa kapena kunena zimene zinapangitsa kuti achedwe. Komanso anayenera kupereka ulemu kwa mayi anga.”

 N’zoona kuti kuchita chinthu chokhumudwitsa kamodzi kokha kapena ngati munthuyo ali ndi khalidwe lina lokhumudwitsa si ndiye kuti chibwenzi chanu chithe. (Salimo 130:3) Koma Sarah atazindikira kuti John nthawi zonse ankachita zinthu mwamwano anaganiza zothetsa chibwenzi.

 Kodi mungatani ngati mofanana ndi Jill komanso Sarah mwaona kuti munthu amene muli naye pachibwenzi siwoyenera kumanga naye banja? Ngati zili choncho simuyenera kungokhala osachita chilichonse. Ngakhale kuti zimakhala zovuta koma ndi nzeru kuthetsa chibwenzicho. Lemba la Miyambo 22:3 limanena kuti: “Wochenjera ndi amene amati akaona tsoka amabisala.”

 Kunena zoona, kuthetsa chibwenzi n’kovuta. Koma muzikumbukira kuti mukalowa m’banja ndi munthuyo mukuyenera kukhala naye kwa moyo wanu wonse. Choncho ndi bwino kudandaula kwa nthawi yochepa panopa chifukwa chakuti mwathetsa chibwenzi m’malo momadzanong’oneza bongo muli m’banja.