Pitani ku nkhani yake

ZIMENE ACHINYAMATA AMAFUNSA

N’chifukwa Chiyani Ndimangolankhula Zolakwika?

N’chifukwa Chiyani Ndimangolankhula Zolakwika?

 “Nthawi zina ndimatha kulamulira lilime langa, koma nthawi zina ndimangolankhula zinthu popanda kuganiza.”—James.

 “Ndikakhala ndi mantha ndimangolankhula zinthu popanda kuganiza kaye ndipo ndikasangalala ndimalankhula zambirimbiri. Choncho ndinganene kuti nthawi zonse ndimavutika kudziletsa polankhula.”—Marie.

 Baibulo limanena kuti: ‘Lilime ndi moto ndipo kamoto kakang’onong’ono kamayatsa nkhalango yaikulu.’ (Yakobo 3:5, 6) Kodi zimene mumalankhula zimakubweretserani mavuto? Ngati zili choncho nkhaniyi ingakuthandizeni.

 N’chifukwa chiyani ndimalankhula zolakwika?

 Si ife angwiro. Baibulo limanena kuti: “Tonsefe timapunthwa nthawi zambiri. Ngati wina sapunthwa pa mawu, ameneyo ndi munthu wangwiro.” (Yakobo 3:2) Popeza si ife angwiro, timapunthwanso mosavuta tikamalankhula osati poyenda pokha.

 “Ubongo wanga komanso lilime langa si zangwiro choncho si nzeru kuganiza kuti ndingamalankhule zabwino zokhazokha.”Anna.

 Kulankhula kwambiri. Baibulo limanena kuti: “Pakachuluka mawu sipalephera kukhala zolakwa.” (Miyambo 10:19) Anthu amene amalankhula kwambiri koma osamvetsera akhoza kukhumudwitsa ena mosavuta.

 “Kulankhula kwambiri sikumasonyeza kuti munthu ndi wanzeru. Yesu ndi munthu wanzeru kwambiri amene anakhalapo padzikoli koma nthawi zina ankakhala chete.”—Julia.

 Kukonda kugemula anthu mowanyoza. Baibulo limanena kuti: “Pali munthu amene amalankhula mosaganizira ndi mawu olasa ngati lupanga.” (Miyambo 12:18) Njira imodzi ya kulankhula mosaganizira ndi kugemula anthu mowanyoza kwambiri. Anthu amene amachita zimenezi anganene kuti, “Ndimangocheza.” Koma kunyoza anthu ena si kosangalatsa. Baibulo limanena kuti ‘mawu achipongwe komanso zoipa zonse zichotsedwe mwa inu.’—Aefeso 4:31.

 “Ndimakonda nthabwala komanso kugemula anthu choncho nthawi zina ndimapezeka kuti ndikunena zinthu zokhumudwitsa ena.”—Oksana.

Simungabweze mawu amene mwalankhula chifukwa zimakhala ngati mwafinya mankhwala otsukira mano omwe simungawabwezere

 Muzilamulira lilime

 Kuphunzira kulamulira lilime si kophweka koma mfundo za m’Baibulo zingatithandize. Mwachitsanzo, taganizirani mfundo zotsatirazi.

 “Lankhulani mumtima mwanu . . . ndipo mukhale chete.”—Salimo 4:4.

 Nthawi zina ndi bwino kungokhala chete. Mtsikana wina dzina lake Laura anati: “Mmene ndimamvera ndikapsa mtima si mmene ndimamvera mtima ukakhala m’malo. Nthawi zambiri ndimasangalala kuti sindinanene zimene ndinkafuna kunena pa nthawiyo.” Munthu akangodikira pang’ono chabe asanalankhule, akhoza kupewa kunena zinthu zolakwika.

 “Kodi khutu si paja limasiyanitsa mawu ngati mmene m’kamwa mumasiyanitsira kakomedwe ka chakudya?”—Yobu 12:11.

 Mukhoza kupewa mavuto ambiri mukamadzifunsa mafunso otsatirawa musanalankhule:

  •   Kodi zimene ndikufuna kulankhulazi n’zoona? Kodi n’zachikondi? Kodi n’zofunika kunena?—Aroma 14:19.

  •   Nanga ndingamve bwanji munthu atanena zomwezo kwa ineyo?Mateyu 7:12.

  •   Kodi zisonyeza kuti ndikulemekeza maganizo a munthuyu?—Aroma 12:10.

  •   Kodi ndi nthawi yabwino yonenera zimenezi?—Mlaliki 3:7.

 ‘Modzichepetsa, muziona ena kukhala okuposani.’—Afilipi 2:3.

 Malangizo amenewa angakuthandizeni kuti muziona anthu ena moyenera. Ndiye mukatero mudzatha kulamulira lilime lanu n’kumaganiza kaye musanalankhule. Ngakhale mutalankhula zinthu zopweteka, kudzichepetsa kungakuthandizeni kuti mupepese mwamsanga. (Mateyu 5:23, 24) Kenako mungamayesetse kulamulira lilime lanu.