Pitani ku nkhani yake

ZIMENE ACHINYAMATA AMADZIFUNSA

Kodi Ndingakulitse Bwanji Luso Lolankhulana Ndi Anthu?

Kodi Ndingakulitse Bwanji Luso Lolankhulana Ndi Anthu?

 N’chifukwa chiyani ndiyenera kulankhulana ndi anthu pamasom’pamaso?

 Anthu ena amaona kuti ndi zovuta komanso zochititsa mantha kulankhulana ndi anthu pamasom’pamaso poyerekezera ndi kulemberana mameseji.

 “Zimakhala zovuta kusintha zomwe wanena ukamalankhulana ndi anthu pamasom’pamaso chifukwa sungakonze kapena kufufuta chilichonse pa zomwe wanena.”​—Anna.

 “Kulemberana mameseji kuli ngati kuonera pulogalamu yojambulidwa kale pomwe kulankhulana pamasom’pamaso kuli ngati kuonera pulogalamu yomwe ikuchitika nthawi yomweyo. Nthawi zonse ndikamalankhulana ndi munthu pamasom’pamaso ndimadziuza kuti, ‘Bwinotu ndisalakwitsepo apa!’”​—Jean.

 Komabe, pa nthawi ina, mudzafunikabe kukhala ndi luso lolankhulana ndi anthu pamasom’pamaso. Mwachitsanzo, mudzafunika kukhala ndi luso limeneli kuti mupeze mabwenzi atsopano, ntchito komanso kuti mukhalitse pa ntchitopo, kapenanso mukamadzafuna kuyamba chibwenzi nthawi yanu ikadzakwana.

 Komabe, simukufunika kuchita mantha kuti muyamba bwanji kukambirana ndi munthu pamasom’pamaso. Mukhoza kuphunzira kuchita zimenezi ngakhale kuti ndinu wamanyazi.

 “Tonsefe nthawi zina timalakwitsa polankhula ndipo timachita manyazi. Choncho, musamayembekezere kuti simukufunika kulakwitsa chilichonse.”​—Neal.

 Ndingayambe bwanji kukambirana ndi anthu?

  •   Muzifunsa mafunso. Ganizirani nkhani imene ingasangalatse anthu kenako yambani kukambirana nawo za nkhaniyo. Mwachitsanzo:

     “Kodi holide yapitayi anzathu munapita kuti?”

     “Webusaitiyi ndi yabwino kwambiri. Kodi munaionapo?”

     “Kodi mwamva zomwe zachitika . . . ?”

     Kuti musavutike kuyamba kukambirana ndi munthu, ganizirani zinthu zina zimene mumachitira limodzi ndi munthuyo. Mwachitsanzo, kodi mumaphunzira sukulu limodzi kapenanso kugwirira ntchito limodzi? Mungagwiritse ntchito zimenezi kuti mupeze poyambira.

     “Muziganizira mafunso amene inuyo mumawaona kuti ndi ochititsa chidwi komanso amene mungakonde kumva mayankho ake kuchokera kwa anthu ena.”​—Maritza.

     Chenjezo: Muzipewa kufunsa mafunso ambirimbiri nthawi imodzi moti mpaka munthu kuchita kuvutika kukuyankhani. Komanso musamafunse mafunso omwe angachititse munthu manyazi. Mafunso monga akuti, “Mudzakwatira liti?” kapenanso “N’chifukwa chiyani nthawi zonse mumavala chovala chomwechomwecho?” angachititse kuti munthu amangike. Funso lachiwirilo lingachititse munthu kuona ngati mukumuimba mlandu.

     Muyeneranso kupewa kufotokoza maganizo anu munthu wina asanayambe kuyankha funso lomwe mwamufunsa kapenanso akangomaliza kumene. Choncho, njira yabwino ndi yoti muzikambirana ndi munthu m’malo momupanikiza ndi mafunso.

    Kodi mumakonda kufunsa mafunso opanikiza anthu ena?

     Mfundo ya m’Baibulo: “Maganizo amumtima mwa munthu ali ngati madzi akuya, koma munthu wozindikira ndi amene amawatunga.”​—Miyambo 20:5.

  •   Muzimvetsera mwatcheru. Kuti mukwanitse kumalankhulana bwino ndi anthu, muzimvetsera mwatcheru m’malo momalankhula kwambiri.

     “Ndimayesetsa kuphunzira chinachake chatsopano chokhudza munthu amene ndikulankhula naye. Kenako, sindimaiwala zimene wandifotokozera ndipo zimenezi zimandithandiza kuti ndipeze funso lomwe ndingadzamufunse tikamadzachezanso ulendo wina.”​—Tamara.

     Chenjezo: Musadere nkhawa kuti ulendo wotsatira mudzanena zotani. Muzingomvetsera mwatcheru basi, ndipo simungavutike kunena zinazake kuchokera pa zimene munthu wina wakufotokozerani.

     Mfundo ya m’Baibulo: “Munthu aliyense azikhala wokonzeka kumvetsera, aziganiza kaye asanalankhule komanso asamafulumire kukwiya.”​—Yakobo 1:19.

  •    Muzichita chidwi ndi ena. Mukamachita chidwi ndi anthu, m’pamene mungamasangalale kwambiri kucheza nawo.

     “Mukamamvetsera mwatcheru zimene munthu wina akufotokoza, mumasonyeza kuti mukuchita naye chidwi ndipo zimathandiza kuti muzisangalala kucheza naye ngakhale kuti nthawi zina mukhoza kumachita manyazi.”​—Marie.

     Chenjezo: Musamalankhule mopitirira malire. Mwachitsanzo, kunena kuti, “Mwavalatu juzi yokongola. Ndiye munaigula ndalama zingati? kungakhale kupitirira malire.

     Mfundo ya m’Baibulo: “Musamaganizire zofuna zanu zokha, koma muziganiziranso zofuna za ena.”​—Afilipi 2:4.

 Kodi mungalankhule mawu otani pomaliza zimene mukukambirana? Mnyamata wina dzina lake Jordan ananena kuti, “Muziyesetsa kumaliza ndi mawu osangalatsa. Mwina munganene kuti, ‘Ndasangalala kwambiri kucheza nanu’, kapena ‘Ndikufunirani tsiku labwino.’ Zimenezi zingathandize kuti mudzapeze poyambira ulendo wina mukadzakumananso.”