Pitani ku nkhani yake

ZIMENE ACHINYAMATA AMADZIFUNSA

Kodi Ndingatani Kuti Ndisamapse Mtima?

Kodi Ndingatani Kuti Ndisamapse Mtima?

 Kuyankha Mafunso

  •  Kodi mumapsa mtima kangati?

    •  sindipsa mtima kwenikweni

    •  mwa apo ndi apo

    •  tsiku lililonse

  •  Kodi mumapsa mtima bwanji?

    •  pang’ono

    •  kwambiri

    •  koopsa

  •  Kodi ndani amakupsetsani mtima nthawi zambiri?

    •  makolo

    •  m’bale wanga

    •  mnzanga

 Ngati muli ndi vuto lopsa mtima, nkhaniyi ikuthandizani. Choyamba, tiyeni tione chifukwa chake simuyenera kupsa mtima.

 Kodi nkhaniyi ndi yofunika bwanji?

 Thanzi lanu. Lemba la Miyambo 14:30 limati: “Mtima wodekha ndiwo moyo wa munthu.” Koma magazini ina imati: “Kupsa mtima kungachititse kuti munthu azidwala matenda a mtima.”—Journal of Medicine and Life.

 Anzanu. Baibulo limati: “Usamagwirizane ndi munthu aliyense wokonda kukwiya, ndipo usamayende ndi munthu waukali.” (Miyambo 22:24) Choncho ngati mumakonda kupsa mtima, musamadabwe ngati anthu safuna kucheza nanu. Mtsikana wina dzina lake Jasmine anati: “Ngati simutha kugwira mtima wanu, mukhoza kumavutika kupeza anzanu abwino.”

 Mmene ena amakuonerani. Mnyamata wina wazaka za 17 dzina lake Ethan anati: “Ngati mwapsa mtima, anthu ena amadziwa zimenezi ndipo akhoza kusintha mmene amakuonerani.” Ndiyeno mudzifunse kuti, ‘Kodi ndimafuna kuti anthu azindiona bwanji? Ndimafuna kuti azindiona kuti ndine munthu wodekha, wabwino kucheza naye kapena munthu wamtima wapachala?’ Baibulo limati: “Wosafulumira kukwiya n’ngozindikira zinthu kwambiri, koma wokwiya msanga amalimbikitsa uchitsiru.”—Miyambo 14:29.

Palibe amene amafuna kucheza ndi munthu amene sachedwa kupsa mtima

 Zimene mungachite

 Taganizirani malemba otsatirawa ndiponso zimene ena ananena, kenako dzifunseni mafunso amene ali m’munsi mwake.

  •   Miyambo 29:22: “Munthu wokonda kukwiya amayambitsa mkangano, ndipo aliyense wokonda kupsa mtima amakhala ndi machimo ambiri.”

     “Pamene ndinali ndi zaka 13 kapena 14, ndinkavutika kwambiri kuugwira mtima. Achibale a bambo anga ali ndi vuto lomweli. Timaona kuti vutoli ndi chibadwa cha ku banja lathu. Tonse kwathu zimativuta kuti tisamapse mtima.”—Kerri.

     Kodi ineyo ndimafulumira kupsa mtima? Ngati ndimanyadira zinthu zimene ndimachita bwino, kodi ndi bwino kungonena kuti zimene sindichita bwino n’chibadwa changa basi?

  •   Miyambo 15:1: “Kuyankha modekha kumabweza mkwiyo, koma mawu opweteka amayambitsa mkwiyo.”

     “Chofunika ndi kumayesetsa kuugwira mtima basi. Mukamayesetsa kukhala munthu wodekha n’kumaganizira zinthu zabwino zimene munthu akuchita, simungafulumire kupsa mtima.”—Daryl.

     N’chifukwa chiyani chinthu choyamba chimene ndimachita munthu akandiyamba, chimakhala chofunika kwambiri?

  •   Miyambo 26:20: “Popanda nkhuni moto umazima.”

     “Ndikachita zinthu mwachikondi pamene munthu wina wandiyamba, nthawi zambiri zimamukhazika mtima pansi munthuyo. Ndiyeno timatha kukambirana popanda kupsetsana mtima.”—Jasmine.

     Kodi zomwe ndingalankhule kapena kuchita zingakulitse bwanji vutolo?

  •   Miyambo 22:3: “Wochenjera ndi amene amati akaona tsoka amabisala, koma anthu osadziwa zinthu amangopitabe ndipo amalangidwa.”

     “Nthawi zina ndimangochokapo kuti ndiganizire bwino zimene zachitikazo. Kenako ndikhoza kuthana ndi vutolo mtima uli m’malo.”​—Gary.

     Kodi ndi nthawi iti imene ingakhale yabwino kuchokapo popanda kusonyeza kuti mwamukwiyira mnzanuyo?

  •   Yakobo 3:2: “Tonsefe timapunthwa nthawi zambiri.”

     “N’zoona kuti timadandaula tikalakwitsa, koma tiyenera kuphunzirapo kanthu pa zimene talakwitsazo. Sitiyenera kutaya mtima koma kungoyesetsa kuti tisalakwitsenso.”​—Kerri.

 Zimene zingakuthandizeni: Khalani ndi cholinga choti pa nthawi inayake, mwina pa mwezi umodzi, muziyesetsa kukhala wodekha. Ndiyeno muzilemba mmene mukuchitira pokwaniritsa cholinga chanuchi.